× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 LUKA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 1234567891011121314151617181920212223241 1 1 : 1 12345678910111213141516171819202122232425262728293031323334353637383940414243444546474849505152535455565758596061626364656667686970717273747576777879801 1 1 Buku Lopatulika LUKA 1 Sungani Zolemba 1POPEZA ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinacitika pakati pa ife,2monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,3kuyambira paciyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira paciyambi, kulembera kwa iwe tsatane tsatane, Teofilo wabwinotu iwe;4kuti udziwitse zoona zace za mau amene unaphunzira.5Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti.6Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa.7Ndipo analibe mwana, popeza Elisabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.8Ndipo panali, pakucita iye nchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu, monga mwa macitidwe a kupereka nsembe,9adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kacisi wa Ambuye.10Ndipo khamu lonse la anthu Iinalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.11Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.12Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.13Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.14Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwace.15Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.16Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.17Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.18Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ici ndi ciani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zace za mkazi wanga zacuruka.19Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, ine ndine Gabrieli, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.20Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzacitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau, anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yace.21Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kucedwa kwace m'kacisimo.22Koma m'mene iye anaturukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kacisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.23Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wace anamarizidwa, anamuka kunyumba kwace.24Ndipo atatha masiku awa, Elisabeti mkazi wace anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,25Ambuye wandicitira cotero m'masiku omwe iye anandipenyera, kucotsa manyazi anga pakati pa anthu.26Ndipo mwezi wacisanu ndi cimodzi mngelo Gabrieli anatumidwa ndi Mulungu kunka ku mudzi wa ku Galileya dzina lace N azarete,27kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lace Yosefe, wa pfuko la Davine; ndipo dzina lace la namwaliyo ndilo Mariya.28Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wocitidwa cisomo, Ambuye ali ndi iwe.29Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulankhula uku nkutani.30Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Mariya; pakuti wapeza cisomo ndi Mulungu.31Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamucha dzina lace Yesu.32Iye adzakhala wamkuru, nadzachedwa Mwana wa Wamkurukuru: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wacifumu wa Davine atate wace:33ndipo iye adzacita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wace sudzatha.34Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?35Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.36Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wace; ndipo mwezi uno uli wacisanu ndi cimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.37Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.38Ndipo Mariya anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anacoka kwa iye.39Ndipo Mariya ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi cangu ku dziko la mapiri ku mudzi wa Yuda;40nalowa m'nyumba ya Zakariya, nalankhula Elisabeti.41Ndipo panali pamene Elisabeti anamva kulankhula kwace kwa Mariya, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwace; ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;42nakweza mau ndi mpfuu waukuru, nati, 2 Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo codalitsika cipatso ca mimba yako,43Ndipo ici cicokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amace wa Ambuye wanga?44Pakuti ona, pamene mau a kulankhula kwako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.45Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; cifukwa zidzacitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.463 Ndipo Mariya anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye,47Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.48Cifukwa iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wace; Pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzandichula ine wodala.49Cifukwa iye Wamphamvuyo anandicitira ine zazikuru; 4 Ndipo dzina lace liri loyera.505 Ndipo cifundo cace cifikira anthu a mibadwo mibadwo Pa iwo amene amuopa iye.51Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace; 6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,52iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yacifumu, Ndipo anakweza aumphawi,537 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, Ndipo eni cuma anawacotsa opanda kanthu.54Anathangatira Israyeli mnyamata wace, Kuti akakumbukile cifundo,558 (Monga analankhula kwa makolo athu) Kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace ku nthawi yonse.56Ndipo Mariya anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwace.57Ndipo inakwanira nthawi ya Elisabeti, ya kubala kwace, ndipo anabala mwana wamwamuna.58Ndipo anansi ace ndi abale ace anamva kuti Ambuye anakulitsa cifundo cace pa iye; 9 nakondwera naye pamodzi.59Ndipo panali 10 tsiku lacisanu ndi citatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amuche dzina la atate wace Zakariya.60Ndipo amace anayankha, kuti, lai; koma 11 adzachedwa Yohane.61Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene achedwa dzina ili.62Ndipo anakodola atate wace, afuna amuche dzina liti?63Ndipo iye anafunsa colemberapo, nalemba, kuti, Dzina lace ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.64Ndipo 12 pomwepo panatseguka pakamwa pace, ndi lilume lace linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.65Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko: lonse la mapiri a Yudeya,66Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.67Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,68Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli; 14 Cifukwa iye anayang'ana, nacitira anthu ace ciombolo,69Ndipo iye anatikwezera ife nyanga ya cipulumutso, Mwa pfuko la Davine mwana wace,7015 (Monga iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe),71Cipulumutso ca adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife;7216 Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukila pangano lace lopatulika;73Cilumbiro cimene iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu,74Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu, 17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,7518 M'ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse.7619 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu: 20 Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace;77Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso, 21 Ndi makhululukidwe a macimoao,78Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;7922 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.80Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika LUKA 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/luke/001.mp3 24 1