× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 AROMA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 123456789101112131415161 1 1 : 6 12345678910111213141516171819202122232425262728293031321 1 1 Buku Lopatulika AROMA 1 Sungani Zolemba 1PAULO, kapolowa Yesu Kristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,2umene iye analonjeza kale ndi mau a ananeri ace m'malembo oyera,3wakunena za Mwana wace, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,4amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu;5amene ife tinalandira naye cisomo ndi utumwi, kuti amvere cikhulupiriro anthu a mitundu yonse cifukwa ca dzina lace;6mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Kristu;7kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.8Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi.9Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wace, kuti kosalekeza ndikumbukila inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga,10ngati nkutheka tsopano mwa cifuniro ca Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.11Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;12ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa cikhulupiriro ca ife tonse awiri, canu ndi canga.13Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.14Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.15Cotero, momwe ndingakhoze ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.16Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.17Pakuti m'menemo caonetsedwa cilungamoca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.18Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wocokera Kumwamba, uonekera pa cisapembedzo conse ndi cosalungama ca anthu, amene akanikiza pansi coonadi m'cosalungama cao;19cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.20Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;21cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,22Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;23nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi cifaniziro ca munthu woonongeka ndi ca mbalame, ndi ca nyama zoyendayenda, ndi ca zokwawa.24Cifukwa cace Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kucititsana matupi ao wina ndi mnzace zamanyazi;25amenewo anasandutsa coonadi ca Mulungu cabodza napembedza, natumikira colengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.26Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe:27ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.28Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;29anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, cinyengo, udani;30akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, acipongwe, odzitama, amatukutuku, ovamba zoipa, osamvera akuru ao,31opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda cikondi ca cibadwidwe, opanda cifundo;32amene ngakhale adziwa kuweruza kwace kwa Mulungu, kuti iwo 2 amene acita zotere ayenera imfa, azicita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzicita.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika AROMA 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/romans/001.mp3 16 1