× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kabardian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong Tibetian South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chisunda Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Bagri Bhilali Bodo Braj Tulu Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Mazanderani Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dagbani Edo Kituba Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 AROMA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 15 123456789101112131415161 1 1 : 5 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132331 1 1 Buku Lopatulika AROMA 15 Sungani Zolemba 1Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.2Yense wa ife akondweretse mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa.3Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe Inagwa pa Ine,4Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.5Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;6kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.7Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.8Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,9ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa, Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, Ndidzayimbira dzina lanu.10Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.11Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; Ndipo anthu onse amtamande.12Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, Ndi iye amene aukira kucita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.13Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.14Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzace.15Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, cifukwa ca cisomo capatsidwa kwa ine ndi Mulungu,16kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.17Cifukwa cace ndiri naco codzitamandira ca m'Kristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.18Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,19mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;20ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.21Koma monga kwalembedwa, Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona, Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.22Cifukwa cacenso ndinaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;23koma tsopano, pamene ndiribe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,24pamene pali ponse ndidzapita ku Spanya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.25Koma 1 tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndirikutumikira oyera mtima.26Pakuti 2 kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kucereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.27Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. 3 Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikica iwo ndi zinthu zathupi.28Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.29Ndipo 4 ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwace kwa cidalitso ca Kristu.30Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;31kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;326 kuti ndi cimwemwe ndikadze kwa inu mwa cifuno ca Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.33Ndipo 7 Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika AROMA 15 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/romans/015.mp3 16 15