× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 AROMA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 8 123456789101112131415161 1 1 : 39 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738391 1 1 Buku Lopatulika AROMA 8 Sungani Zolemba 1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.5Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:6pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.8Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi;13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,15Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,16Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;17ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.18Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.19Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.20Pakuti colengedwaco cagonietsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca iye amene anacigonjetsa,21ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wa cibvundi, ndi kolowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,22Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.23Ndipo si cotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu.24Pakuti ife tinapolumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pa kuti ayembekezera ndani cimene acipenya?25Koma ngati tiyembekezera cimene: siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.26Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;27ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.28Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.29Cifukwa kuti iwo 1 amene iye anawadziwiratu, 2 iwowa anawalamuliratu 3 afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti 4 iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;30ndipo amene iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene iye anawayesa olungama, 5 iwowa anawapatsanso olemerero.31Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? 6 Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?32iye amene sanatimana Mwana wace wa iye yekha, koma 7 anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?33Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? 8 Mulungu ndiye ameneawayesa olungama;349 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife.35Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?36Monganso kwalembedwa, 12 Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse; Tinayesedwa monga nkhosa zakupha,37Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.38Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu,39ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika AROMA 8 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/romans/008.mp3 16 8