× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 Buku Lopatulika 2014 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MASALIMO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 105 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253545556575859606162636465666768697071727374757677787980818283848586878889909192939495969798991001011021031041051061071081091101111121131141151161171181191201211221231241251261271281291301311321331341351361371381391401411421431441451461471481491501 1 1 : 37 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344451 1 1 Buku Lopatulika MASALIMO 105 Sungani Zolemba 1Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye.2Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse.3Mudzitamandire ndi dzina lake loyera: mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.4Funani Yehova, ndi mphamvu yake; funsirani nkhope yake nthawi zonse.5Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita; zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake;6inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake.7Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu; maweruzo ake akhala pa dziko lonse lapansi.8Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;9chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki;10ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele.11Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholandira chako;12pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;13nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena.14Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa.15Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.16Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate.17Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:18Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka m'unyolo;19kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa.20Mfumuyo anatuma munthu nammasula; woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.21Anamuika akhale woyang'anira nyumba yake, ndi woweruza wa pa zake zonse:22Amange nduna zake iye mwini, alangize akulu ake adziwe nzeru.23Pamenepo Israele analowa m'Ejipito; ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.24Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake, nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.25Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.26Anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aroni amene adamsankha.27Anaika pakati pao zizindikiro zake, ndi zodabwitsa m'dziko la Hamu.28Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake.29Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, naphanso nsomba zao.30Dziko lao linachuluka achule, m'zipinda zomwe za mafumu ao.31Ananena, ndipo inadza mitambo ya ntchentche, ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.32Anawapatsa mvula yamatalala, lawi la moto m'dziko lao.33Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao; nathyola mitengo kufikira m'malire ao onse.34Ananena, ndipo linadza dzombe ndi mphuchi, ndizo zosawerengeka,35ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao, zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.36Ndipo Iye anapha achisamba onse m'dziko mwao, choyambira cha mphamvu yao yonse.37Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.38Ejipito anakondwera pakuchoka iwo; popeza kuopsa kwao kudawagwera.39Anayala mtambo uwaphimbe; ndi moto uunikire usiku.40Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.41Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi; nayenda pouma ngati mtsinje.42Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake.43Potero anatulutsa anthu ake ndi kusekerera, osankhika ake ndi kufuula mokondwera.44Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:45Kuti asamalire malemba ake, nasunge malamulo ake. Aleluya.Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi Buku Lopatulika MASALIMO 105 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/psalms/105.mp3 150 105