× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kabardian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong Tibetian South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chisunda Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Madurese Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Bagri Bhilali Bodo Braj Tulu Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Mazanderani Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dagbani Edo Kituba Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 Buku Lopatulika 2014 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MASALIMO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 106 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253545556575859606162636465666768697071727374757677787980818283848586878889909192939495969798991001011021031041051061071081091101111121131141151161171181191201211221231241251261271281291301311321331341351361371381391401411421431441451461471481491501 1 1 : 6 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647481 1 1 Buku Lopatulika MASALIMO 106 Sungani Zolemba 1Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha.2Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?3Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.4Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu:5Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.6Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa.7Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu m'Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.8Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti adziwitse chimphamvu chake.9Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.10Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani.11Ndipo madziwo anamiza owasautsa; sanatsale mmodzi yense.12Pamenepo anavomereza mau ake; anaimbira chomlemekeza.13Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake:14Popeza analakalakatu kuchidikhako, nayesa Mulungu m'chipululu.15Ndipo anawapatsa chopempha iwo; koma anaondetsa mitima yao.16Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova.17Dziko lidayasama nilidameza Datani, ndipo linafotsera gulu la Abiramu.18Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto; lawi lake lidapsereza oipawo.19Anapanga mwanawang'ombe ku Horebu, nagwadira fano loyenga.20M'mwemo anasintha ulemerero wao ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu.21Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao, amene anachita zazikulu m'Ejipito;22zodabwitsa m'dziko la Hamu, zoopsa ku Nyanja Yofiira.23Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge.24Anapeputsanso dziko lofunika, osavomereza mau ake;25koma anadandaula m'mahema mwao, osamvera mau a Yehova.26Potero anawasamulira dzanja lake, kuti awagwetse m'chipululu:27Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.28Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori, nadyanso nsembe za akufa.29Ndipo anamkwiyitsa nazo zochita zao; kotero kuti mliri unawagwera.30Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango: Ndi mliriwo unaletseka.31Ndipo adamuyesa iye wachilungamo, ku mibadwomibadwo kunthawi zonse.32Anautsanso mkwiyo wake kumadzi a Meriba, ndipo kudaipira Mose chifukwa cha iwowa:33Pakuti anawawitsa mzimu wake, ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yake.34Sanaononga mitunduyo ya anthu, imene Yehova adawauza;35koma anasokonekerana nao amitundu, naphunzira ntchito zao:36Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha:37Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,38nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.39Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.40Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake, nanyansidwa Iye ndi cholowa chake.41Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.42Adani ao anawasautsanso, nawagonjetsa agwire mwendo wao.43Iye anawalanditsa kawirikawiri; koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao, ndi mphulupulu zao zinawafoketsa.44Koma anapenya nsautso yao, pakumva kufuula kwao:45Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.46Ndipo anawachitira kuti apeze nsoni pamaso pa onse amene adawamanga ndende.47Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, ndi kutisokolotsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.48Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi Buku Lopatulika MASALIMO 106 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/psalms/106.mp3 150 106