× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 Buku Lopatulika 2014 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 LEVITIKO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 19 1234567891011121314151617181920212223242526271 1 1 : 31 123456789101112131415161718192021222324252627282930313233343536371 1 1 Buku Lopatulika LEVITIKO 19 Sungani Zolemba 1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,2Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.3Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.4Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.5Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.6Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto.7Akakadya konse tsiku lachitatu kali chonyansa, kosavomerezeka:8koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.9Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.10Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.11Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.12Musamalumbira monama ndi kutchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.13Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.14Usamatemberera wogontha; usamaika chokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.15Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.16Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.17Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.18Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.19Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.20Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.21Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopalamula.22Ndipo wansembe achite chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula pamaso pa Yehova, chifukwa cha kuchimwa adachimwaku; ndipo adzakhululukidwa chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwaku.23Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.24Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova.25Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.26Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.27Musamameta mduliro, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu.28Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova.29Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi.30Muzisunga masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.31Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.32Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.33Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.34Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.35Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake.36Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.37Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi Buku Lopatulika LEVITIKO 19 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/leviticus/019.mp3 27 19