× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 Buku Lopatulika 2014 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 YOHANE GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 6 1234567891011121314151617181920211 1 1 : 27 12345678910111213141516171819202122232425262728293031323334353637383940414243444546474849505152535455565758596061626364656667686970711 1 1 Buku Lopatulika YOHANE 6 Sungani Zolemba 1Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.2Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.3Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi ophunzira ake.4Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira.5Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?6Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita.7Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.8Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,9Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?10Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.11Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.12Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.13Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo.14Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.15Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.16Koma pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira kunyanja;17ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.18Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako.19Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.20Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope.21Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.22M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;23koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;24chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.25Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti?26Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.27Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.28Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?29Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.30Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?31Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya.32Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.33Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.34Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.35Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.36Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.37Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.38Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.39Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza.40Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.41Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.42Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?43Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze wina ndi mnzake.44Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.45Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.46Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.47Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha.48Ine ndine mkate wamoyo.49Makolo anu adadya m'chipululu, ndipo adamwalira.50Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.51Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.52Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?53Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.54Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.55Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.56Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.57Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.58Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.59Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao.60Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?61Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?62Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?63Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.64Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.65Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.66Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye.67Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka?68Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.69Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.70Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?71Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi Buku Lopatulika YOHANE 6 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/john/006.mp3 21 6