× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 Buku Lopatulika 2014 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 AROMA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 9 123456789101112131415161 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132331 1 1 Buku Lopatulika AROMA 9 Sungani Zolemba 1Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbu mtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,2kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.3Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;4ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;5a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.6Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;7kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.8Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.9Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.10Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;11pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,12chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.13Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.14Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.15Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.16Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.17Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.18Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.19Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuno chake?20Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?21Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?22Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?23Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero,24ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?25Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.26Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.27Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.28Pakuti Ambuye adzachita mau ake pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule.29Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.30Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsata chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;31koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikila lamulolo.32Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsata ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;33monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi Buku Lopatulika AROMA 9 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/romans/009.mp3 16 9