× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 2016 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MASALIMO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 106 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253545556575859606162636465666768697071727374757677787980818283848586878889909192939495969798991001011021031041051061071081091101111121131141151161171181191201211221231241251261271281291301311321331341351361371381391401411421431441451461471481491501 1 1 : 6 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647481 1 1 Mawu a Mulungu MASALIMO 106 Sungani Zolemba 1 Tamandani Yehova. Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.2Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?3Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.4Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu, bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,5kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika, kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.6Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.7Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.8Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.9Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma; anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.10Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo; anawawombola mʼdzanja la mdani.11Madzi anamiza adani awo, palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.12Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.13Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake.14Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.15Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa.16Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.17Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani; inakwirira gulu la Abiramu.18Moto unayaka pakati pa otsatira awo; lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.19Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.20Anasinthanitsa ulemerero wawo ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.21Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa, amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,22zozizwitsa mʼdziko la Hamu ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.23Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga, pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa, kuyima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.24Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.25Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo ndipo sanamvere Yehova.26Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake, kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,27kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.28Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;29anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa, ndipo mliri unabuka pakati pawo.30Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo, ndipo mliri unaleka.31Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake, kwa mibado yosatha imene ikubwera.32Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,33pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu, ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.34Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu monga momwe Yehova anawalamulira.35Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo ndi kuphunzira miyambo yawo.36Ndipo anapembedza mafano awo, amene anakhala msampha kwa iwowo.37Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.38Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.39Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita; ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.40Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.41Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina, ndipo adani awo anawalamulira.42Adani awo anawazunza ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.43Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri, koma iwo ankatsimikiza za kuwukira ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.44Koma Iye anaona kuzunzika kwawo pamene anamva kulira kwawo;45Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.46Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo awamvere chisoni.47Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu, ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera ndi kunyadira mʼmatamando anu.48Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, Kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Ameni!” Tamandani Yehova.Chewa Bible 2016 The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.® Mawu a Mulungu MASALIMO 106 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/106.mp3 150 106