Baibulo mu chaka chimodzi Okutobala 10YEREMIYA 5:1-311. Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ace, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakucita zolungama, wakufuna coonadi; ndipo ndidzamkhululukira.2. Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.3. Yehova Inu, maso anu sali pacoonadi kodi? munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwa mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.4. Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena ciweruzo ca Mulungu wao.5. Ine ndidzanka kwa akuru, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi ciweruzo ca Mulungu wao. Koma awa anabvomerezana natyola gori, nadula zomangira zao.6. Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.7. Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.8. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wace.9. Kodi sindidzawalanga cifukwa ca zimenezi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu woterewu?10. Kwerani pa makoma ace nimupasule; koma musatsirize konse; cotsani nthambi zace pakuti siziri za Yehova.11. Pakuti nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zinandicitira monyenga kwambiri, ati Yehova.12. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; coipa sicidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;13. ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; comweco cidzacitidwa ndi iwo.14. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa makamu atero, Cifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.15. Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutari, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene cinenero cace simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.16. Phodo lao liri ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba.17. Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako amuna ndi akazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.18. Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.19. Ndipo padzakhala: pamene mudzati, Cifukwa canji Yehova Mulungu wathu aticitira ife zonse izi? ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yacilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko siliri lanu.20. Nenani ici m'nyumba ya Yakobo, lalikirani m'Yuda, kuti,21. Tamvanitu ici, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;22. Kodi simundiopa Ine? ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mcenga cilekaniro ca nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? ndipo ngakhale mafunde ace acita gabvigabvi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.23. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nacoka.24. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yace; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.25. Mphulupulu zanu zacotsa zimenezi, ndi zocimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.26. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.27. Monga cikwere codzala ndi mbalame, comweco nyumba zao zadzala ndi cinyengo; cifukwa cace akula, alemera,28. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kucita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.29. Sindidzawalanga kodi cifukwa ca zimenezi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu wotere?30. Codabwitsa ndi coopsya caoneka m'dzikomo;31. aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzacita ciani pomarizira pace?YEREMIYA 6:1-301. Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekoa, kwezani cizindikiro m'Beti-hakeremu; pakuti caoneka coipa coturuka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.2. Ndidzacotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.3. Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pace.4. Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.5. Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zace.6. Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwace modzala nsautso.7. Monga kasupe aturutsa madzi ace, camweco aturutsa zoipa zace; ciwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwace; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.8. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.9. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.10. Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.11. Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.13. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita monyenga,14. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.15. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita conyansa? lai, sanakhala konse ndi manyazi, sanathe kunyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika cwa iwo, aclzagwetsedwa, ati Yehova.16. Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.17. Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera.18. Cifukwa cace tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, cimene ciri mwa iwo.19. Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera coipa pa anthu awa, cipatso ca maganizo ao, pakuti sanamvera mau anga, kapena cilamulo canga, koma wacikana.20. Cofukiza cindifumiranji ku Seba, ndi nzimbe ku dziko lakutari? nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.21. Cifukwa cace atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zopunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzace adzatayika.22. Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu ucokera kumpoto; ndi mtundu waukuru adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.23. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.24. Tamva ife mbiri yace; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.25. Usaturukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.26. Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udzibveke ndi ciguduli, ndi kubvimbvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.27. Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.28. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi citsulo; onsewa acita mobvunda;29. mbvukuto yatenthedwa ndi moto; mthobvu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga cabe; pakuti oipa sacotsedwa.30. Anthu adzawacha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.MASALIMO 117:1-21. Lemekezani Yehova, amitundu onse; Myimbireni, anthu onse.2. Pakuti cifundo cace ca pa ife ndi cacikuru; Ndi coonadi ca Yehova ncosatha. Haleluya.MIYAMBO 27:3-43. Mwala ulemera, mcenga ndiwo katundu; Koma mkwiyo wa citsiru upambana kulemera kwace.4. Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; Koma ndani angalakike ndi nsanje?AKOLOSE 1:1-291. PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,2. kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Kristu a m'Kolose: Cisomo kwa inu ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu.3. Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi kupempherera Inu nthawi zonse,4. popeza tidamva za cikhulupiriro canu ca mwa Kristu Yesu, ndi cikondi muli naco kwa oyera mtima onse;5. cifukwa ca ciyembekezo cosungikira kwa inu m'Mwamba, cimene mudacimva kale m'mau a coonadi ca Uthenga Wabwino,6. umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu; kuyambira tsikulo mudamva nimunazindildra cisomo ca Mulungu m'coonadi;7. monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiyemtumiki wokhulupirika wa Kristu cifukwa ca ife;8. amenenso anatifotokozera cikondi canu mwa Mzimu.9. Mwa ici ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi cizindikiritso ca cifuniro cace mu nzeru zonse ndi cidziwitso ca mzimu,10. kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu nchito yonse yabwino, ndi kukula m'cizindikiritso ca Mulungu;11. olimbikitsidwa m'cilimbiko conse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wace, kucitira cipiriro conse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi cimwemwe,12. ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao colowa ca oyera mtima m'kuunika;13. amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa cikondi cace;14. amene tiri nao maomboledwe mwa iye, m'kukhululukidwa kwa zocimwa zathu;15. amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse;16. pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.17. Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.18. Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba.19. Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire,20. mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.21. Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'cifuwa canu m'nchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani22. m'thupi lace mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda cirema ndi osatsutsika pamaso pace;23. ngatitu mukhalabe m'cikhulupiriro, ocirimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana naco ciyembekezo ca Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa colengedwa conse ca pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wace.24. Tsopano 1 ndikondwera nazo zowawazo cifukwa ca inu, ndipo 2 ndikwaniritsa zoperewera za cisautso ca Kristu m'thupi langa 3 cifukwa ca thupi lace, ndilo Eklesiayo;25. amene ndinakhala mtumiki wace, 4 monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakucitira inti, wakukwaniritsa mau a Mulungu,26. 5 ndiwo cinsinsico cinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anacionetsa tsopano kwa oyera mtima ace,27. kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ici 6 cimene ciri cuma ca ulemerero wa cinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Kristu mwa inu, ciyembekezo ca ulemerero;28. amene timlalikira ife, ndi kucenjeza munthu ali yense 7 ndi kuphunzitsa munthu ali yense mu nzeru zonse, 8 kuti tionetsere munthu ali yense wamphumphu mwa Kristu;29. kucita ici ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa 9 monga mwa macitidwe ace akucita mwa ine ndi mphamvu. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society