Baibulo mu chaka chimodzi
Okutobala 5

1. Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwakutsegulidwa kwa m'ndende;
2. ndikalalikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
3. ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, cobvala ca matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
4. Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.
5. Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa.
6. Koma inu mudzachedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya cuma ca amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.
7. M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi citonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; cifukwa cace iwo adzakhala naco m'dziko mwao colowa cowirikiza, adzakhala naco cikondwerero cosatha.
8. Pakuti Ine Yehova ndikonda ciweruziro, ndida cifwamba ndi coipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.
9. Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.
10. Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandibveka ine ndi zobvala za cipulumutso, nandipfunda copfunda ca cilungamo, monga mkwati abvala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
11. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zace, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa cilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.
1. Cifukwa ca Ziyoni sindidzakhala cete, ndi cifukwa ca Yerusalemu sindidzapuma, kufikira cilungamo cace cidzaturuka monga kuyera, ndi cipulumutso cace monga nyali yoyaka.
2. Ndipo amitundu adzaona cilungamo cako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzachedwa dzina latsopano, limene m'kamwa mwa Yehova mudzachula.
3. Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wacifumu m'dzanja la Mulungu wako.
4. Iwe sudzachedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzachedwanso Bwinja; koma iwe udzachedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.
5. Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako amuna adzakukwama iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.
6. Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala cete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale cete,
7. ndipo musamlole akhale cete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi.
8. Yehova analumbira pa dzanja lace lamanja, ndi mkono wace wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale cakudya ca adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira nchito;
9. koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamchera adzamumwa m'mabwalo a kacisi wanga.
10. Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; cotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.
11. Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona cipulumutso cako cifika; taona mphotho yace ali nayo, ndi nchito yace iri pamaso pace.
12. Ndipo iwo adzawacha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzachedwa Wofunidwa, Mudzi wosasiyidwa.
9. Israyeli, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
10. Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao.
11. Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
12. Yehova watikumbukila; adzatidalitsa: Adzadalitsa nyumba ya Israyeli; Adzadalitsa nyumba ya Aroni.
13. Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, Ang'ono ndi akuru.
24. Wakuda mnzace amanyenga ndi milomo yace; Koma akundika cinyengo m'kati mwace;
25. Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire; Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26. Angakhale abisa udani wace pocenjera, Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.
1. Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ici ncabwino.
2. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),
3. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikuru padziko.
4. Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi cilangizo ca Ambuye.
5. Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila kanthu kena, monga kwa Kristu;
6. si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima;
7. akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;
8. podziwa kuti cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.
9. Ndipo, ambuye inu, muwacitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankhu kwa iye.
10. Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.
11. Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika pokana macenjerero a mdierekezi.
12. Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m'zakumwamba.
13. Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.
14. Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo;
15. ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;
16. koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro, cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo.
17. Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;
18. mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
19. ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu cinsinsico ca Uthenga Wabwino,
20. cifukwa ca umene 1 ndiri mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.
21. Koma 2 kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndicita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tukiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;
22. amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca icico, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.
23. 3 Mtendere ukhale kwa abale, ndi cikondi, pamodzi ndi cikhulupiriro, zocokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Kristu.
24. Akhale naco cisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Kristu m'eosaonongeka.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society