Baibulo mu chaka chimodzi Okutobala 8YEREMIYA 1:1-191. MAU a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;2. amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wace wa Amoni, mfumu ya Ayuda caka cakhumi ndi citatu ca ufumu wace.3. Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wace wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi cimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wacisanu.4. Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,5. Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.6. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.7. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena conse cimene ndidzakuuza.8. Usaope nkhope zao; cifukwa Ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.9. Ndipo Yehova anaturutsa dzanja lace, na'khudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;10. penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse; umange, ubzyale.11. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona ntyole ya katungurume.12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwacita.13. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti, ona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pace unafulatira kumpoto.14. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kucokera kumpoto coipa cidzaturukira onse okhala m'dziko.15. Pakuti, taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wacifumu wace pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda.16. Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, nagwadira nchito za manja ao.17. Koma iwe ukwinde m'cuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.18. Cifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wacitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akuru ace, ndi pa ansembe ace, ndi pa anthu a m'dziko.19. Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; cifukwa Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.YEREMIYA 2:1-371. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,2. Pita nupfuule n'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, cikondi ca matomedwe ako; muja unanditsata m'cipululu m'dziko losabzya lamo.3. Israyeli anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zace; onse amene adzamudya iye adzayesedwa oparamula; coipa cidzawagwera, ati Yehova.4. Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israyeli;5. atero Yehova, Atate anu apeza cosalungama canji mwa Ine, kuti andicokera kunka kutari, natsata zacabe, nasanduka acabe?6. Osati, Ali kuti Yehova amene anatikweza kucokera ku dziko la Aigupto, natitsogolera m'cipululu, m'dziko loti se ndi la maenje, m'dziko la cirala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitamo anthu, losamangamo anthu?7. Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zace, ndi zabwino zace; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa colandira canga conyansa.8. Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.9. Cifukwa cace ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.10. Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati cinalipo cotere.11. Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siiri milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi cosapindula.12. Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova.13. Pakuti anthu anga anacita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.14. Kodi Israyeli ndi mtumiki? kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? afunkhidwa bwanji?15. Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lace, midzi yace yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.16. Ananso a Nofi ndi a Tahapanesi, anaswa pakati pamtu pako.17. Kodi sunadzicitira ici iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?18. Tsopano uli naco ciani m'njira ya ku Aigupto, kumwa madzi a Sihori? uli naco ciani m'njira ya ku Asuri, kumwa madzi a m'Nyanja?19. Coipa cako cidzai kulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ici ndi coipa ndi cowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.20. Pakuti kale lomwe ndinatyola gori lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitari, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kucita dama.21. Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pace, ya mpesa wacilendo?22. Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.23. Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'cigwa, dziwa cimene wacicita; ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m'njira zace;24. mbidzi yozolowera m'cipululu, yopumira mphepo pakufuna pace; pokomana nayo ndani adzaibweza? onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wace.25. Kaniza phazi lako lisakhale losabvala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe ciyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.26. Monga mbala iri ndi manyazi pamene igwidwa, comweco nyumba ya Israyeli iri ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akuru ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;27. amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kubvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.28. Koma iri kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kubvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, Yuda iwe.29. Cifukwa canji mudzatsutsana ndi Ine nonse? mwandilakwira Ine, ati Yehova.30. Ndapanda ana anu mwacabe; sanamvera kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.31. Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israyeli cipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Cifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?32. Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zace, kapena mkwatibwi zobvala zace? koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.33. Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna cilakolako? cifukwa cace waphunzitsa akazi oipa njira zako.34. Ndiponso m'nsaru zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osacimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.35. Koma unati, Ndiri wosacimwa ndithu; mkwiyo wace wacoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, cifukwa uti, Sindinacimwa.36. Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? udzacitanso manyazi ndi Aigupto monga unacita manyazi ndi Asuri.37. Koma udzaturuka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.MASALIMO 116:5-145. Yehova ngwa cifundo ndi wolungama; Ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.6. Yehova asunga opusa; Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa,7. Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; Pakuti Yehova anakucitira cokoma.8. Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa, Maso anga kumisozi, Mapazi anga, ndingagwe.9. Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo.10. Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula; Ndinazunzika kwambiri.11. Pofulumizidwa mtima ndinati ine, Anthu Onse nga mabodza.12. Ndidzabwezera Yehova ciani Cifukwa ca zokoma zace zonse anandicitira?13. Ndidzanyamula cikho ca cipulumutso, Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova,14. Ndidzacitazowindazanga za kwa Yehova, Tsopano, pamaso pa anthu ace onse.MIYAMBO 27:1-11. Usanyadire zamawa, Popeza sudziwa tsiku lina lidzabala ciani?AFILIPI 3:1-211. Cotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.2. Penyererani agaru, penyererani ocita zoipa, penyererani coduladula;3. pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;4. ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;5. wodulidwa tsiku lacisanu ndi citatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa pfuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;6. monga mwa cangu, wolondalonda Eklesia; monga mwa cilungamo ca m'lamulo wokhala wosalakwa ine.7. Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa citayiko cifukwa ca Kristu.8. Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu,9. ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;10. kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu ya kuuka kwace, ndi ciyanjano ca zowawa zace, pofanizidwa ndi imfa yace;11. ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.12. Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.13. Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,14. ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.15. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;16. cokhaci, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.17. Abale khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife citsanzo canu.18. Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawiri kawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Kristu;19. citsiriziro cao ndico kuonongeka, mulungu wao ndiyo niimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amenealingirira za padziko.20. Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu;21. amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society