Baibulo mu chaka chimodzi February 13EKSODO 37:1-291. Ndipo Bezaleli anapanga likasa la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;2. ndipo analikuta ndi golidi woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.3. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi pa miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace imodzi, ndi mphete: ziwiri pa mbali yace yina.4. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.5. Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.6. Ndipo anapanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.7. Anapanganso akerubi awiri agolidi; anacita kuwasula mapangidwe ace, pa mathungo ace swiri a coteteze rapo;8. kerubi mmodzi pa mbali yace imodzi, ndi kerubi wilia pa mbali yace yina; anapanga akerubi ocokera m'cotetezerapo, pa mathungo ace awiri.9. Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba cotetezerapo ndi mao piko ao, ndi nkhope zao zopeoyana; zinapenya kucotetezerapo nkhope zao.10. Ndipo anapanga gome la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri, ndi kupingasa kwace mkono limodzi, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;11. ndipo analikuta ndi golidi woona, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.12. Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira anapangirapo mkombero wagolidi.13. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi, naika mphetezo pa ngondya zace zinai zokhala pa miyendo yace inai.14. Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo.15. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndigolidi, kunyamulira nazo gomelo.16. Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo, za golidi woona.17. Ndipo anapanga coikapo nyali ca golidi woona; mapangidwe ace a coikapo nyalico anacita cosula, tsinde lace ndi thupi lace, zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zinakhala zocokera m'mwemo;18. ndi m'mbali zace munaturuka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace imodzi, ndi mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace yina;19. pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda yina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyali.20. Ndipo pa coikapo nyali comwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;21. ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mweno, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zocokera m'mwemo.22. Mitu yao ndi mphanda zao zinaturuka m'mwemo; conseci cinali cosulika pamodzi ca golidi woona.23. Ndipo anapanga nyali zace zisanu ndi ziwiri ndi mbano zace, ndi zoolera zace, za golidi woona.24. Anacipanga ici ndi zipangizo zace zonse za talente wa golidi woona.25. Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wasitimu; utali wace mkono, ndi kupingasa kwace mkono, lampwamphwa; ndimsinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zinaturuka m'mwemo.26. Ndipo analikuta ndi golidi woona, pamwamba pace, ndi mbali zace pozungulira, ndi nyanga zace; ndipo analipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.27. Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolidi pansi pa mkombero wace, pa ngondya zace ziwiri, pa mbali zace ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.28. Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.29. Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi cofukiza coona ca pfungo lokoma, mwa macitidwe a wosanganiza.EKSODO 38:1-311. Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono itaru.2. Ndipo anapanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zinakhala zoturuka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.3. Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zoparira moto; zipangizo zace zonse anazipanga zamkuwa.4. Ndipo anapangira guwa La nsembelo made, malukidwe ace nja mkuwa, pansi pa matso ace wakulekeza pakati pace.5. Ndipo anayengera mathungo anai a made amkuwawo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko.6. Napanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi mkuwa.7. Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.8. Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la cihema cokomanako.9. Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwela, kumwela, nsaru zocingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;10. nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zasiliva.11. Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsici zace makumi awiri, nw makamwa ace makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.12. Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsaru zocingira za mikono makumi asanu, nsid zace khumi, ndi makamwa ace khumi; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.13. Ndi pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mikono makumi asanu.14. Nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya cipata nza mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu;15. momwemonso pa mbali yina: pa mbali yino ndi pa mbali yina ya cipata ca pabwalo panali nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu.16. Nsaru zocingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.17. Ndipo makamwa a nsici anali amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda Iyace zasiliva; ndi zokutira mitu yace zasiliva; ndi nsici zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.18. Ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo ndiyo nchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mu kupingasa kwace mikono isanu, yolingana ndi nsaru zocingira za pabwalo.19. Ndi nsici zace zinali zinai, ndi makamwa ace anai, amkuwa; zokowera zace zasiliva, ndi zokutira mitu yace ndi mitanda yace zasiliva.20. Ndi ziciri zonse za cihema, ndi za bwalo lace pozungulira, nza mkuwa.21. Ici ndi ciwerengo ca zinthu za cihema, cihema ca mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, acite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.22. Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose.23. Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.24. Golidi yense anacita naye mu nchito yonse ya malo opatulika, golidi wa coperekaco, ndico matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.25. Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli cikwi cimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika;26. munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kumka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.27. Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsaru yocinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.28. Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsici ndi masekeli aja cikwi cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yace, nazigwirizitsana pamodzi.29. Ndi mkuwa wa coperekaco ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.30. Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ace amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,31. ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku cipata ca pabwalo, ndi ziciri zonse za cihema, ndi ziciri zonse za pabwalo pozungulira.MASALIMO 22:9-159. Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa: Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.10. Cibadwire ine anandisiyira Inu: Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.11. Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi: Pakuti palibe mthandizi.12. Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga: Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,13. Andiyasamira m'kamwa mwao, Ngati mkango wozomola ndi wobangula.14. Ndathiridwa pansi monga madzi, Ndipo mafupa anga onse anaguluka: Mtima wanga ukunga sera; Wasungunuka m'kati mwa matumbo anga,15. Mphamvu yanga yauma ngati phale; Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga; Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.MIYAMBO 8:12-2112. Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga; Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.13. Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.14. Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa; Ndine luntha; ndiri ndi mphamvu.15. Mwa ine mafumu alamulira; Akazembe naweruza molungama.16. Mwa ine akalonga ayang'anira, Ndi akuru, ngakhale oweruza onse a m'dziko,17. Akundikonda ndiwakonda; Akundifunafuna adzandipeza.18. Katundu ndi ulemu ziri ndi ine, Cuma cosatha ndi cilungamo.19. Cipatso canga ciposa golidi, ngakhale golidi woyengeka; Phindu langa liposa siliva wosankhika.20. Ndimayenda m'njira ya cilungamo, Pakati pa mayendedwe a ciweruzo,21. Kuti ndionetse cuma akundikonda, cikhale colowa cao, Ndi kudzaza mosungira mwao.MATEYU 26:51-7551. Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.52. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,53. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?54. Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera comweco?55. Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munaturukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wacifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kacisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.56. Koma izi zonse zinacitidwa, kuti 1 zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.57. Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.58. Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.59. Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;60. koma sanaupeza zingakhale 2 mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pace anadza awiri,61. nati, Uyu ananena kuti, 3 Ndikhoza kupasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu.62. Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?63. Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.64. Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, 5 Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.65. Pomwepo mkuru wa ansembe 6 anang'amba zobvala zace, nati, Acitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? onani, tsopano mwamva mwanowo;66. muganiza bwanji? lwo anayankha nati, 7 Ali woyenera kumupha,67. 8 Pomwepo iwo anathira malobvu pankhope pace, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda kofu,68. nati, 9 Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?69. Ndipo 10 Petro adakhala pabwato: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.70. Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Cimene unena sindicidziwa.71. Ndipo pamene iye anaturuka kunka kucipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.72. Ndipo anakananso ndi cilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo.73. Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.74. 11 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.75. Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, 12 Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society