Baibulo mu chaka chimodzi Marichi 17NUMERI 31:1-541. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,2. Abwezereni cilango Amidyani cifukwa ca ana a Israyeli; utatero udzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wako.3. Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidyani, kuwabwezera Amidyani cilango ca Yehova.4. Muwatume kunkhondo a pfuko limodzi, cikwi cimodzi, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, atere mafuko onse a Israyeli.5. Ndipo anapereka mwa zikwi za Israyeli, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.6. Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.7. Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.8. Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.9. Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.10. Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.11. Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.12. Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.13. Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anaturuka kukomana nao kunja kwa cigono.14. Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.15. Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?16. Taonani, awa analakwitsa ana a Israyeli pa Yehova nilica Peoricija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.17. Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.18. Koma ana akazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeru ndi moyo akhale anu.19. Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ali yense adapha munthu, ndi ali yense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lacitatu ndi lacisanu ndi ciwiri, inu ndi andende anu.20. Muyeretse zobvala zanu zonse, zipangizo zonse zacikopa, ndi zaomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse zamtengo.21. Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la cilamuloco Yehova analamulira Mose ndi ili:22. Golidi, ndi siliva, mkuwa, citsulo, ndolo ndi mtobvu zokha,23. zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.24. Ndipo muzitsuke zobvala zanu tsiku lacisanu ndi ciwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'cigono.25. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,26. Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe; ndi Eleazara wansembe, ndi akuru a nyumba za makolo za khamulo;27. nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anaturuka kunkhondo, ndi khamu lonse.28. Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akuturuka kunkhondo apereke kwa Yehova; munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.29. Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.30. Ndipo ku gawo la ana a Israyeli utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova.31. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anacita monga Yehova anamuuza Mose.32. Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,33. ndi ng'ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,34. ndi aburu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu cimodzi,35. ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri.36. Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adaturuka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.37. Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.38. Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.39. Ndipo aburu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.40. Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.41. Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.42. Ndipo kunena za gawo la ana a Israyeli, limene Mose adalicotsa kwa anthu ocita nkhondowo,43. (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,44. ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi,45. ndi aburu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,46. ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi,)47. mwa gawolo la ana a Israyeli Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.48. Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;49. nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowa munthu mmodzi wa ife.50. Ndipo tabwera naco copereka ca Yehova, yense cimene anacipeza, zokometsera zagolidi, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kucita cotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.51. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golidiyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.52. Ndipo golidi yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.53. Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.54. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golidi kwa akuru a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku cihema cokomanako, cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova.NUMERI 32:1-421. Koma ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazeri, ndi dziko la Gileadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.2. Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,3. Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazeri, ndi Nimra, ndi Heseboni, ndi Eleyali, ndi Sebamu, ndi Nebo, ndi Beoni,4. dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israyeli, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.5. Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale lao lao; tisaoloke Yordano.6. Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?7. Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israyeli kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?8. Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza acoke ku Kadesi Barinea kukaona dziko.9. Popeza atakwera kumka ku cigwa ca Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israyeli, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.10. Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira iye, nati,11. Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;12. koma Kalebi mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.13. Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israyeli, nawayendetsa-yendetsa m'cipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udacita coipa pamaso pa Yehova.14. Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ocimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israyeli,15. Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata iye, adzawasiyanso m'cipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.16. Ndipo anayandikiza, nati, Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israyeli, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao;17. ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga cifukwa ca okhala m'dzikomo.18. Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israyeli atalandira yense colowa cace.19. Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordano, ndi m'tsogolo mwace; popeza colowa cathu tacilandira tsidya lino la Yordano kum'mawa.20. Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzacita ici, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,21. ndi kuoloka Yordano pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapitikitsa adani ace pamaso pace,22. ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osacimwira Yehova ndi Israyeli; ndipo dziko ili lidzakhala lanu lanu pamaso pa Yehova.23. Koma mukapanda kutero, taonani, mwacimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti cimo lanu lidzakupezani.24. Dzimangireni midzi ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzicite zoturuka m'kamwa mwanu.25. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzacita monga mbuyanga alamulira.26. Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Gileadi;27. koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.28. Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akuru a makolo a mapfuko a ana a Israyeli za iwo.29. Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordano, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Gileadi likhale lao lao;30. koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko ao ao pakati pa inu m'dziko la Kanani.31. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzacita.32. Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma colowa cathu cathu cikhale tsidya lino la Yordano.33. Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi pfuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, dzikoli ndi midzi yace m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako,34. Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroeri;35. Ataroti Sofani, Yazeri, ndi Yogebeha;36. ndi Beti Nimira, ndi Beti Harani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta.37. Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyali, ndi Kiriyataimu;38. ndi Nebo, ndi Baala Meoni (nasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaicha midzi adaimanga ndi maina ena.39. Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase anamka ku Gileadi, naulanda, napitikitsa Aamori anali m'mwemo.40. Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Gileadi; ndipo anakhala m'menemo.41. Ndipo Yairi mwana wa Manase anamka nalanda midzi yao, naicha Havoti Yairi. Ndipo Noba anamka nalanda Kenati, ndi miraga yace, naucha Noba, dzina lace.42. Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova: Limbanani nao iwo akulimbana nane.MASALIMO 35:1-81. Gwirani cikopa cocinjiriza, Ukani kundithandiza.2. Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola: Nenani ndi moyo wanga, Cipulumutso cako ndine.3. Athe nzeru nacite manyazi iwo akufuna moyo wanga: Abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira ciwembu.4. Akhale monga mungu kumphepo, Ndipo mngelo wa Yehova awapitikitse.5. Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera, Ndipo mngelo wa Yehova awalondole.6. Pakuti anandichera ukonde wao m'mbunamo kopanda cifukwa, Anakumbira moyo wanga dzenje kopanda cifukwa.7. Cimgwere modzidzimutsa cionongeko; Ndipo ukonde wace umene anaucha umkole yekha mwini: Agwemo, naonongeke m'mwemo.8. Wokonda mwambo akonda kudziwa; Koma wakuda cidzudzulo apulukira.MIYAMBO 12:1-11. Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.MARKO 14:55-7255. Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana.56. Ndipo ananyamukapo ena, namcitira umboni wakunama, nanena kuti,57. Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.58. Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana.59. Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?60. Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka?61. Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.62. Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?63. Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.64. Ndipo ena mayamba kumthira malobvu Iye, adi kuphimba nkhope yace, ndi cumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo ananpanda Iye kofu.65. Ndipo pamene Petro anali iansi m'bwalo, anadzapo mmodzi va adzakazi a mkulu wa ansembe;66. ndipo anaona Petro alikuotha noto, namyang'ana iye, nanena, wenso unali naye Mnazarene, Yesu.67. Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa cimene ucinena iwe; ndipo anaturuka kunka kucipata; ndipo tambala analira.68. Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.69. Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uti Mgalileya.70. Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.71. Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society