Baibulo mu chaka chimodzi Juni 152 MAFUMU 17:1-411. Caka cakhumi ndi ziwiri ca Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.2. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israyeli asanakhale iye.3. Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.4. Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.5. Pamenepo mfumu ya Asuri anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.6. Caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Asuri analanda Samariya, natenga Aisrayeli andende, kumka nao ku Asuri; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.7. Kudatero, popeza ana a Israyeli adacimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwaturutsa m'dziko la Aigupto pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anaopa milungu yina,8. nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli, ndi m'miyambo ya mafumu a Israyeli imene iwo anawalangiza.9. Ndipo ana a Israyeli anacita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse ku nsanja ya olonda ndi ku mudzi walinga komwe.10. Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa citunda ciri conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira;11. nafukizapo zonunkhira pa misanje youse, monga umo amacitira amitundu amene Yehova adawacotsa pamaso pao, nacita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;12. natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musacita ici.13. Ndipo Yehova anacitira umboni Israyeli ndi Yuda mwa dzanja la mneneri ali yense, ndi mlauli ali yense, ndi kuti, Bwererani kuleka nchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa cilamulo conse ndinacilamulira makolo anu, ndi kucitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.14. Koma sanamvera, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirira Yehova Mulungu wao.15. Ndipo anakaniza malemba ace, ndi cipangano anacicita ndi makolo ao, ndi mboni zace anawacitira umboni nazo, natsata zopanda pace, nasanduka opanda pace, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asacite monga iwowa.16. Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, ana a ng'ombe awiri, napanga cifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.17. Napititsa ana ao amuna ndi akazi kumoto, naombeza ula, nacita zanyanga, nadzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.18. Cifukwa cace Yehova anakwiya naye Israyeli kwakukuru, nawacotsa pamaso pace osatsala mmodzi, koma pfuko la Yudalokha.19. Yudansosanasunga malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israyeli amene adawaika.20. Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israyeli, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pace.21. Pakuti anang'amba Israyeli, kumcotsa ku nyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati; Yerobiamu naingitsa Israyeli asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukuru.22. Nayenda ana a Israyeli m'zolakwa zonse za Yerobiamu, zimene anazicita osazileka;23. mpaka Yehova adacotsa Israyeli pamaso pace, monga adanena mwa dzanja la atumiki ace onse aneneriwo. Momwemo Israyeli anacotsedwa m'dziko lao kumka nao ku Asuri mpaka lero lino.24. Ndipo mfumu ya Asuri anabwera nao anthu ocokera ku Babulo, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Safaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israyeli; nakhala iwo eni ace a Samariya, nakhala m'midzi mwace.25. Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaopa Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.26. Motero ananena ndi mfumu ya Asuri, kuti, Amitundu aja mudawacotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; cifukwa cace anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, irikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.27. Pamenepo mfumu ya Asuri analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawacotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.28. Nadza wina wa ansembewo adawacotsa ku Samariya, nakhala ku Beteli, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova.29. Koma a mtundu uli wonse anapanga milungu yao yao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uli wonse m'midzi mwao mokhala iwo.30. Ndipo anthu a Babulo anapanga Sukoti Bemoti, ndi anthu a Kuta anapanga Nerigali, ndi anthu a Hamati anapanga Asima,31. ndi Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.32. Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.33. Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawacotsako.34. Mpaka lero lino acita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sacita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena cilamulo, kapena coikika adacilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamucha Israyeli,35. ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu yina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;36. koma Yehova amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;37. ndi malemba, ndimaweruzo, ndi cilamulo, ndi coikika anakulemberani muzisamalira kuzicita masiku onse, nimusamaopa milungu: yina;38. ndi cipangano ndinacicita nanu musamaciiwala, kapena kuopa milungu yina iai;39. koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.40. Koma sanamvera, nacita monga mwa mwambo wao woyamba.41. Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anacita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.2 MAFUMU 18:1-371. Ndipo kunali caka cacitatu ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu waceo2. Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Abi mwana wa Zekariya.3. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita Davide kholo lace.4. Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.5. Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.6. Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.7. Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.8. Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.9. Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.10. Pakutha pace pa zaka zitatu anaulanda, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Israyeli analanda Samariya.11. Ndipo mfumu ya Asuri anacotsa Aisrayeli kumka nao ku Asuri, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;12. cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.13. Caka cakhumi ndi zinai ca Hezekiya Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.14. Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.15. Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba yamfumu.16. Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golidi wa pa zitseko za Kacisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asuri.17. Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.18. Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawaturukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolemba mbiri.19. Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Cikhulupiriro ici ncotani ucikhulupirira?20. Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?21. Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Aigupto; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lace ndi kulibola; atero Farao mfumu ya Aigupto kwa onse omkhulupirira iye.22. Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamcotsera misanje yace ndi maguwa a nsembe ace, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pane m'Yerusalemu?23. Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.24. Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Aigupto akupatse magareta ndi apakavalo?25. Ngati ndakwerera malo ana wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.26. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.27. Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?28. Naima kazembeyo, napfuula ndi mau akulu m'Ciyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikuru mfumu ya Asuri.29. Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m'dzanja lace;30. kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mudzi uwu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.31. Musamvere Hezekiya; pakuti Itero mfumu ya Asuri, Mupangane nane zamtendere, nimuturukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wace, ndi yense ku mkuyu wace, ndi kumwa yense madzi a m'citsime cace;32. mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uci; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.33. Kodi mlungu uli wonse wa amitundu walanditsa dziko lace m'dzanja la mfumu ya Asuri ndi kale lonse?34. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?35. Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?36. Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.37. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.MASALIMO 74:1-81. Mulungu, munatitayiranji citayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?2. Kumbukilani msonkhano wanu, umene munaugula kale, Umene munauombola ukhale pfuko la colandira canu; Phiri La Ziyoni limene mukhalamo.3. Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha, Zoipa zonse adazicita mdani m'malo opatulika.4. Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu; Aika mbendera zao zikhale zizindikilo.5. Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.6. Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zace zonse Ndi nkhwangwa ndi nyundo,7. Anatentha malo anu opatulika; Anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.8. Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; Anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.MIYAMBO 18:22-2422. Wopeza mkazi apeza cinthu cabwino; Yehova amkomera mtima.23. Wosauka amadandaulira; Koma wolemera ayankha mwaukali.24. Woyanjana ndi ambiri angodziononga; Koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.MACHITIDWE A ATUMWI 1:1-261. TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa,2. kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;3. kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumuwa Mulungu;4. ndipo e posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;5. pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.6. Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?7. Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.8. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.9. Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.10. Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao;11. amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.12. Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kucokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.13. Ndipo pamene adalowa, anakwera ku cipinda ca pamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelote, ndi Yuda mwana wa Yakobo.14. Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Mariya, amace wa Yesu, ndi abale ace omwe.15. Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),16. Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.17. Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.18. (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;19. ndipo cinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanachedwa Akeldama, ndiko, kadziko ka mwazi.)20. Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo, Pogonera pace pakhale bwinja, Ndipo pasakhale munthu wogonapo; Ndipo uyang'aniro wace autenge wina.21. Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,22. kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwace pamodzi ndi ife.23. Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wochedwa Barsaba, amene anachedwanso Yusto, ndi Matiya.24. Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikiramitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,25. alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kucokera komwe Yudase anapatukira, kuti apite ku malo a iye yekha.26. Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiya; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society