Baibulo mu chaka chimodzi Seputembala 18YESAYA 27:1-131. Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.2. Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, yimbani inu za uwo.3. Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.4. Ndiribe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? ndiziponde ndizitenthe pamodzi.5. Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nacite nane mtendere; inde, acite nane mtendere.6. M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israyeli adzaphuka ndi kucita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi.7. Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?8. Munalimbana naye pang'ono, pamene munamcotsa; wamcotsa iye kuomba kwace kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.9. Cifukwa cace, mwa ici coipa ca Yakobo cidzafafanizidwa, ndipo ici ndi cipatso conse cakucotsa cimo lace; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.10. Pakuti mudzi wocingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati cipululu; mwana wa ng'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamariza nthambi zace.11. Ponyala nthambi zace zidzatyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; cifukwa cace Iye amene anawalenga sadzawacitira cisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.12. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wace, kucokera madzi a nyanja, kufikira ku mtsinje wa Aigupto, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israyeli.13. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikuru lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asuri, ndi opitikitsidwa a m'dziko la Aigupto; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.YESAYA 28:1-291. Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'cigwa ca nthaka yabwino.2. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati cimphepo ca matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.3. Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu adzaponderezedwa;4. ndi duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu pa cigwa ca nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kuca malimwe asanafike; polona wakupenya imeneyo, amaidya iri m'dzanja lace.5. Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ace otsala:6. ndipo adzakhala mzimu wa ciweruziro kwa oweruza mirandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pacipata.7. Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi cakumwa caukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza.8. Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udio, palibe malo okonzeka.9. Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere?10. Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.11. Iai, koma ndi anthu a milomo yacilendo, ndi a lilume lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;12. amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.13. Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.14. Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu.15. Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;16. cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.17. Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.18. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kubvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalepereka; popita mliri woopsya udzakuponderezani pansi.19. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; cifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsya kokha, kumva mbiri yace.20. Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi copfunda cacepa, sicingamfikire.21. Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'cigwa ca Gibeoni; kuti agwire nchito yace, nchito yace yacilendo, ndi kuti acite cocita cace, cocita cace cacilendo.22. Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za cionongeko cotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.23. Cherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.24. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? kodi amacocolabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?25. Atakonza tyatyatya pamwamba pace, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza citowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ace osankhika, ndi mcewere m'maliremo?26. Pakuti Mulungu wace amlangiza bwino namphunzitsa.27. Pakuti sapuntha mawere ndi copunthira cakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya gareta pacitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba citowe ndi cibonga.28. Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya gareta wace, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ace sapera.29. Icinso cifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wace uzizwitsa ndi nzeru yace impambana.MASALIMO 107:33-4333. Asanduliza mitsinje ikhale cipululu, Ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma;34. Dziko lazipatso, likhale lakhulo, Cifukwa ca coipa ca iwo okhalamo.35. Asanduliza cipululu cikhale tha wale, Ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.36. Ndi apo akhalitsa anjala, Kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;37. Nafese m'minda, naoke mipesa, Ndiyo vakubata zipatso zolemeza.38. Ndipo awadalitsa, kotero kuti, acuruka kwambiri; Osacepsanso zoweta zao.39. Koma acepanso, nawerama, Cifukwa ca cisautso, coipa ndi cisoni.40. Atsanulira cimpepulo pa akulu, Nawasokeretsa m'cipululu mopanda njira.41. Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, Nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.42. Oongoka mtima adzaciona nadzasekera; Koma cosalungama conse citseka pakamwa pace.43. Wokhala nazo nzeru asamalire izi, Ndipo azindikire zacifundo za Yehova,MIYAMBO 25:20-2020. Monga wobvula maraya tsiku lamphepo, Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.2 AKORINTO 10:1-181. Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Kristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzicepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;2. koma ndipempha kuti pokhala ndiri pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi,3. Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi,4. (pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);5. ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;6. ndi kukhala okonzeka Irubwezera cilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.7. Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Kristu, ayesere icinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Kristu, koteronso ife.8. Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kocurukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye ku kumangirira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;9. kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo.10. Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lace ngofoka, ndi mau ace ngacabe.11. Wotereyo ayese ici kuti monga tiri ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tiri oterenso m'macitidwe pokhala tiri pomwepo.12. Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.13. Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa cilekelezero cimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.14. Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Kristu:15. osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,16. kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwace mwa inu, sikudzitamandira mwa cilekezero ca wina, ndi zinthu zokonzeka kale.17. Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;18. pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka. Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society