2. Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono.
3. Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
4. Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya.
5. Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
6. Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?
7. Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
8. Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.
9. Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse:
10. pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.
11. Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;
12. nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;
13. mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja:
14. Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.
15. Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.
16. Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.
29. Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.
30. Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.
32. Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.
33. Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.
34. Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.
1. Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.
2. Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mau ananena Yosefe.
3. Pamene kudacha, anamukitsa anthu iwo ndi abulu ao.
20. Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.
21. Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.
22. Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa.
23. Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga.
24. Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanu atate wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.
30. Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;
31. kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.
32. Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.
33. Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake.
34. Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga.
1. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?