Baibulo mu chaka chimodzi Okutobala 10YEREMIYA 5:1-311. Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.2. Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.3. Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.4. Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao.5. Ine ndidzanka kwa akulu, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi chiweruzo cha Mulungu wao. Koma awa anavomerezana nathyola goli, nadula zomangira zao.6. Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.7. Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.8. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake.9. Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?10. Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.11. Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.12. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; choipa sichidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;13. ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.14. Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.15. Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.16. Phodo lao lili ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba.17. Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.18. Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.19. Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.20. Nenani ichi m'nyumba ya Yakobo, lalikirani m'Yuda, kuti,21. Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;22. Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.23. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka.24. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.25. Mphulupulu zanu zachotsa zimenezi, ndi zochimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.26. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.27. Monga chikwere chodzala ndi mbalame, chomwecho nyumba zao zadzala ndi chinyengo; chifukwa chake akula, alemera.28. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.29. Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?30. Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m'dzikomo;31. aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?YEREMIYA 6:1-301. Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekowa, kwezani chizindikiro m'Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.2. Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.3. Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake.4. Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.5. Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zake.6. Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso.7. Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.8. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.9. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.10. Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.11. Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.13. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.14. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.15. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.16. Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.17. Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera.18. Chifukwa chake tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, chimene chili mwa iwo.19. Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.20. Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.21. Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.22. Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.23. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.24. Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.25. Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.26. Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kuvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.27. Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.28. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda;29. mvukuto yatenthedwa ndi moto; mtovu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga chabe; pakuti oipa sachotsedwa.30. Anthu adzawatcha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.MASALIMO 117:1-21. Lemekezani Yehova, amitundu onse; muimbireni, anthu onse.2. Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu; ndi choonadi cha Yehova nchosatha. Aleluya.MIYAMBO 27:3-43. Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.4. Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?AKOLOSE 1:1-291. Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,2. kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a m'Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.3. Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse,4. popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse;5. chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu m'Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,6. umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m'choonadi;7. monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife;8. amenenso anatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu.9. Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,10. kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;11. olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,12. ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;13. amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake;14. amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;15. amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;16. pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.17. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.18. Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.19. Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire,20. mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba.21. Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo,22. koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;23. ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.24. Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;25. amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwaniritsa mau a Mulungu,26. ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake,27. kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;28. amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;29. kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu. Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi