2. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israele, Kwatha; kwafika kutha kwake pangodya zinai za dziko.
3. Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.
4. Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5. Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza.
6. Kutha kwafika, kwafika kutha. Kwakugalamukira, taona kwafika.
7. Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku lili pafupi, ndilo laphokoso, si lakufuula mokondwera kumapiri.
8. Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.
9. Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.
10. Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako latuluka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka.
11. Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.
12. Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve chisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wonse.
13. Pakuti wogulitsa sadzabwera ku chogulitsacho, chinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wake wonse sadzapita pachabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wake m'mphulupulu yake.
14. Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wake wonse.
15. Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.
16. Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.
17. Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi.
18. Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.
19. Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.
20. Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.
21. Ndipo ndidzachipereka m'dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m'dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa.
23. Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi chiwawa.
24. Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.
25. Chionongeko chilinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.
26. Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.
27. Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzavala chipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera. Ndidzawachitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
1. Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chimodzi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, tsiku lachisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.
2. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa.
3. Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.
4. Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa Israele, monga mwa maonekedwe ndinawaona kuchidikha chija.
5. Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake.
6. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.
7. Ndipo anadza nane kuchipata cha kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga.
8. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo.
9. Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzichita komweko.
10. M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zilombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israele, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse.
11. Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.
12. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
13. Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikulu zina azichita.
14. Pamenepo anadza nane kuchitseko cha chipata cha nyumba ya Yehova choloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tamuzi.
15. Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzaonanso zonyansa zazikulu zoposa izi.
16. Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.
17. Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.
18. Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera Ine.
1. Nyimbo yokwerera. Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.
2. Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.
5. Tsoka ine, kuti ndili mlendo m'Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!
6. Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.
7. Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.
15. Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
1. Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.
2. Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.
8. Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.
9. Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.
10. Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.
11. Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.
12. Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
13. Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.
14. Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.
15. Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.
16. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.