Baibulo mu chaka chimodzi Ogasiti 8YOBU 7:1-211. Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?2. Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,3. momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake. Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.4. Ndigona pansi, ndikuti, Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira; ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha.5. Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi; khungu langa lang'ambika, nilinyansa.6. Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba, apitirira opanda chiyembekezo.7. Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo, diso langa silidzaonanso chokoma.8. Diso la amene andiona silidzandionanso, maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.9. Mtambo wapita watha, momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.10. Sadzabweranso kunyumba yake, osamdziwanso malo ake.11. Potero sindidzaletsa pakamwa panga; ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga; ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.12. Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m'nyanja, kuti Inu mundiikira odikira?13. Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa, pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa;14. pamenepo mundiopsa ndi maloto, nimundichititsa mantha ndi masomphenya;15. potero moyo wanga usankha kupotedwa, ndi imfa, koposa mafupa anga awa.16. Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo chikhalire; mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.17. Munthu ndani kuti mumkuze, ndi kuti muike mtima wanu pa iye,18. ndi kuti mucheze naye m'mawa ndi m'mawa, ndi kumuyesa nthawi zonse?19. Mukana kundichokera kufikira liti, kapena kundileka mpaka nditameza dovu?20. Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani, Inu wodikira anthu? Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu? Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?21. Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.YOBU 8:1-221. Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,2. Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?3. Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo? Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?4. Chinkana ana ako anamchimwira Iye, ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;5. koma ukafunitsitsa Mulungu, ndi kupembedza Wamphamvuyonse;6. ukakhala woyera ndi woongoka mtima, zoonadi adzakugalamukira tsopano, ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.7. Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono, chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.8. Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo, nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.9. Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a pa dziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;10. amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera, ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?11. Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho? Ngati manchedza amera popanda madzi?12. Akali auwisi, sanawacheke, auma, asanaume mathengo onse ena.13. Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.14. Kulimbika mtima kwake kudzathyoka, chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude.15. Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira; adzaiumirira koma yosakhalitsa.16. Akhala wamuwisi pali dzuwa, ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.17. Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi, apenyerera pokhalapo miyala.18. Akamuononga kumchotsa pamalo pake, padzamkana, ndi kuti, Sindinakuona.19. Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake, ndi panthaka padzamera ena.20. Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa.21. Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka, ndi milomo yako kufuula.22. Iwo akudana nawe adzavala manyazi; ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.MASALIMO 92:8-158. Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.9. Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika.10. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano.11. Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira.12. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.13. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.14. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,15. kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.MIYAMBO 22:17-2117. Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.18. Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako, ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.19. Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi, kuti ukhulupirire Yehova.20. Kodi sindinakulembera zoposa za uphungu ndi nzeru;21. kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?AROMA 9:1-151. Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbu mtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,2. kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.3. Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;4. ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;5. a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.6. Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;7. kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.8. Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.9. Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.10. Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;11. pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,12. chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.13. Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.14. Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.15. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi