Baibulo mu chaka chimodzi Seputembala 10YESAYA 11:1-161. Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;2. Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;3. ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:4. koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.5. Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.6. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.7. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.8. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m'funkha la mphiri.9. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga mdazi adzaza nyanja.10. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.11. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.12. Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.13. Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.14. Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.15. Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.16. Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito.YESAYA 12:1-61. Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.2. Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.3. Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.4. Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.5. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.6. Tafuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.MASALIMO 106:6-186. Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa.7. Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu m'Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.8. Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti adziwitse chimphamvu chake.9. Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.10. Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani.11. Ndipo madziwo anamiza owasautsa; sanatsale mmodzi yense.12. Pamenepo anavomereza mau ake; anaimbira chomlemekeza.13. Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake:14. Popeza analakalakatu kuchidikhako, nayesa Mulungu m'chipululu.15. Ndipo anawapatsa chopempha iwo; koma anaondetsa mitima yao.16. Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova.17. Dziko lidayasama nilidameza Datani, ndipo linafotsera gulu la Abiramu.18. Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto; lawi lake lidapsereza oipawo.MIYAMBO 25:3-53. Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya, koma mitima ya mafumu singasanthulike.4. Chotsera siliva mphala yake, mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale.5. Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.2 AKORINTO 2:1-171. Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.2. Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni?3. Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.4. Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa.5. Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititsa chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse.6. Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira;7. kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.8. Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.9. Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.10. Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu;11. kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.12. Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,13. ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.14. Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.15. Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;16. koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?17. Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu. Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi