Baibulo mu chaka chimodzi Seputembala 8YESAYA 7:1-251. Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.2. Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.3. Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu;4. nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.5. Chifukwa Aramu ndi Efuremu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukuchitira zoipa, nati,6. Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pake, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeele;7. atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzachitidwa.8. Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;9. ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.10. Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,11. Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba.12. Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.13. Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?14. Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.15. Iye adzadya mafuta ndi uchi, pamene adziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino.16. Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.17. Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.18. Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzaimbira mluzu ntchentche ili m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Ejipito, ndi njuchi ili m'dziko la Asiriya.19. Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.20. Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m'mapazi, ndi lumo lobwereka lili tsidya lija la nyanja, kunena mfumu ya Asiriya; ndilo lidzamalizanso ndevu.21. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri;22. ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.23. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.24. Munthu adzafikako ndi mivi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga.25. Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako chifukwa cha kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa.YESAYA 8:1-221. Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakulu, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.2. Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.3. Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.4. Chifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.5. Ndipo Yehova ananena kwa ine kachiwirinso, nati,6. Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang'onopang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;7. chifukwa chake, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a mtsinje wa Yufurate, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asiriya ndi ulemerero wake wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zake zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.8. Ndipo iye adzapitapita kulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake, kudzakwanira dziko lanu m'chitando mwake, inu Imanuele.9. Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka.10. Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.11. Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati,12. Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha.13. Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye.14. Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu.15. Ndipo ambiri adzaphunthwapo, nagwa, nathyoka, nakodwa, natengedwa.16. Manga umboni, mata chizindikiro pachilamulo mwa aphunzi anga.17. Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.18. Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.19. Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?20. Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.21. Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba;22. nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.MASALIMO 105:37-4537. Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.38. Ejipito anakondwera pakuchoka iwo; popeza kuopsa kwao kudawagwera.39. Anayala mtambo uwaphimbe; ndi moto uunikire usiku.40. Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.41. Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi; nayenda pouma ngati mtsinje.42. Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake.43. Potero anatulutsa anthu ake ndi kusekerera, osankhika ake ndi kufuula mokondwera.44. Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:45. Kuti asamalire malemba ake, nasunge malamulo ake. Aleluya.MIYAMBO 24:30-3430. Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru.31. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.32. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo.33. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona,34. ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.1 AKORINTO 16:1-241. Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.2. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.3. Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.4. Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.5. Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya;6. ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.7. Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.8. Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.9. Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.10. Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;11. chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.12. Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.13. Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.14. Zanu zonse zichitike m'chikondi.15. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),16. kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.17. Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.18. Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere.19. Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao.20. Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsona kopatulika.21. Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa.22. Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.23. Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi inu.24. Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen. Chewa Bible 2014 Bible Society of Malawi