Baibulo mu chaka chimodzi Julayi 20EZARA 1:1-111. Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.2. Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.3. Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu.4. Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”5. Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.6. Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija.7. Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.8. Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.9. Chiwerengerochi chinali motere: Mabeseni agolide — 30 mabeseni asiliva — 1,000 a zopereka — 2910. timiphika tagolide — 230 timiphika tasiliva — 410 ziwiya zina — 1,000.11. Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.EZARA 2:1-701. Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.2. Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:3. Zidzukulu za Parosi — 2,1724. zidzukulu za Sefatiya — 3725. zidzukulu za Ara — 7756. zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) — 2,8127. zidzukulu za Elamu — 1,2548. zidzukulu za Zatu — 9459. zidzukulu za Zakai — 76010. zidzukulu za Bani — 64211. zidzukulu za Bebai — 62312. zidzukulu za Azigadi — 1,22213. zidzukulu za Adonikamu — 66614. zidzukulu za Bigivai — 2,05615. zidzukulu za Adini — 45416. zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) — 9817. zidzukulu za Bezayi — 32318. zidzukulu za Yora — 11219. zidzukulu za Hasumu — 22320. zidzukulu za Gibari — 95.21. Anthu a ku Betelehemu — 12322. Anthu aamuna a ku Netofa — 5623. Anthu aamuna a ku Anatoti — 12824. Anthu aamuna a ku Azimaveti — 4225. Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti — 74326. Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba — 62127. Anthu aamuna a ku Mikimasi — 12228. Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai — 22329. Anthu aamuna a ku Nebo — 5230. Anthu aamuna a ku Magaibisi — 15631. Anthu aamuna a ku Elamu wina — 1,25432. Anthu aamuna a ku Harimu — 32033. Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono — 72534. Anthu aamuna a ku Yeriko — 34535. Anthu aamuna a ku Sena — 3,630.36. Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) — 97337. Zidzukulu za Imeri — 1,05238. Zidzukulu za Pasuri — 1,24739. Zidzukulu za Harimu — 1,017.40. Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) — 74.41. Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu — 128.42. Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai — 139.43. Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,44. zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,45. zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,46. zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,47. zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,48. zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,49. zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,50. zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,51. zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,52. zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,53. zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,54. zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.55. Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,56. zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,57. zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.58. Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali — 392.59. Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:60. Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali — 652.61. Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)62. Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo.63. Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.64. Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360,65. kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200.66. Anali ndi akavalo 736, nyulu 245,67. ngamira 435 ndi abulu 6,720.68. Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.69. Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.70. Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.MASALIMO 86:6-106. Yehova imvani pemphero langa; mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.7. Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.8. Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.9. Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.10. Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.MIYAMBO 21:15-1615. Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala, koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.16. Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.MACHITIDWE A ATUMWI 21:18-4018. Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko.19. Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.20. Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose.21. Iwo anawuzidwa kuti iwe umaphunzitsa Ayuda onse amene akukhala pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Mose, kuti asamachite mdulidwe kapena kutsatira miyambo.22. Nanga pamenepa ife titani? Iwo adzamva ndithu kuti iwe wabwera,23. tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu.24. Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo.25. Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”26. Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.27. Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo,28. akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.”29. Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.30. Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata.31. Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka.32. Nthawi yomweyo iye anatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali ndi kuthamangira kumene kunali anthuwo. Anthuwo ataona mkuluyo ndi asilikali ake analeka kumenya Paulo.33. Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani.34. Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali.35. Paulo atafika pa makwerero olowera ku malo a asilikaliwo, ananyamulidwa ndi asilikali chifukwa cha ukali wa anthuwo.36. Gulu la anthu limene linamutsatira linapitiriza kufuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi!”37. Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?” Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki?38. Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”39. Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”40. Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri. Chewa Bible 2016 The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.®