Baibulo mu chaka chimodzi Ogasiti 10YOBU 11:1-201. Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,2. “Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa? Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?3. Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?4. Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’5. Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe6. ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake, pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri. Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.7. “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?8. Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani? Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani?9. Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.10. “Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?11. Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo; akaona choyipa, kodi sachizindikira?12. Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.13. “Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,14. ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,15. udzatukula mutu wako wosachita manyazi; udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.16. Udzayiwala ndithu zowawa zako, zidzakhala ngati madzi amene apita kale.17. Moyo wako udzawala kupambana usana, ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.18. Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo; ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.19. Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.20. Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza, ndipo adzasowa njira yothawirapo; chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”YOBU 12:1-251. Pamenepo Yobu anayankha kuti,2. “Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!3. Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?4. “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!5. Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.6. Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.7. “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;8. kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.9. Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?10. Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.11. Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya?12. Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?13. “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.14. Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.15. Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.16. Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.17. Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza.18. Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.19. Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.20. Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.21. Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.22. Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.23. Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.24. Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.25. Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.MASALIMO 94:1-111. Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango, Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.2. Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera.3. Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova, mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?4. Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.5. Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu.6. Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye.7. Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.”8. Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?9. Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?10. Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?11. Yehova amadziwa maganizo a munthu; Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.MIYAMBO 22:24-2524. Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya25. kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake ndi kukodwa mu msampha.AROMA 10:1-211. Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.2. Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.3. Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.4. Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.5. Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”6. Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu)7. “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa).8. Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,9. kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.10. Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.11. Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”12. Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye13. pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”14. Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?15. Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”16. Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”17. Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.18. Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”19. Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”20. Ndipo Yesaya molimba mtima akuti, “Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”21. Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti, “Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga kwa anthu osandimvera ndi okanika.” Chewa Bible 2016 The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.®