Baibulo mu chaka chimodzi Seputembala 10YESAYA 11:1-161. Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.2. Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.3. Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa. Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva;4. koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.5. Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.6. Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi, mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.7. Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ana awo adzagona pamodzi, ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.8. Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba, ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.9. Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.10. Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero.11. Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.12. Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera, ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli; Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.13. Nsanje ya Efereimu idzatha, ndipo adani a Yuda adzatha; Efereimu sadzachitira nsanje Yuda, ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.14. Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo; ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa. Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu, ndipo Aamoni adzawagonjera.15. Yehova adzaphwetsa mwendo wa nyanja ya Igupto; adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.16. Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira amene anatsalira ku Asiriya, monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli pamene amachokera ku Igupto.YESAYA 12:1-61. Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati: “Ndikukuyamikani, Inu Yehova; chifukwa ngakhale munandipsera mtima, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mwanditonthoza.2. Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga; ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.”3. Mudzakondwera popeza Yehova ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.4. Tsiku limenelo mudzati: “Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.5. Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu; zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.6. Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”MASALIMO 106:6-186. Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.7. Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.8. Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.9. Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma; anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.10. Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo; anawawombola mʼdzanja la mdani.11. Madzi anamiza adani awo, palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.12. Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.13. Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake.14. Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.15. Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa.16. Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.17. Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani; inakwirira gulu la Abiramu.18. Moto unayaka pakati pa otsatira awo; lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.MIYAMBO 25:3-53. Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi, ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.4. Chotsa zoyipa mʼsiliva ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.5. Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu; ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.2 AKORINTO 2:1-171. Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko.2. Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni?3. Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe.4. Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.5. Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera.6. Chilango chimene ambiri a inu mwamupatsa munthu ameneyu nʼchokwanira.7. Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima.8. Choncho ndikukupemphani kuti mutsimikizire chikondi chanu pa iye.9. Cholinga china chimene ndinakulemberani kalata ija chinali chofuna kukuonani ngati mudzandimvera pa zonse.10. Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu,11. kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.12. Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo,13. ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.14. Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.15. Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka.16. Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?17. Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu. Chewa Bible 2016 The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.®