Yerekezerani Baibulo
- |
|---|
| 1 |
| Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo. |
| 2 |
| Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.” |
| 3 |
| Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.” |
| Chewa Bible 2016
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc |
| 1 |
| Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. |
| 2 |
| Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pachika: ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, macimo ako akhululukidwa. |
| 3 |
| Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu acitira Mulungu mwano. |
| Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society |
| 1 |
| Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. |
| 2 |
| Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa. |
| 3 |
| Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano. |
| Chewa Bible 1922
Bible Society of Malawi |
| 1 |
| Yesu adaloŵa m'chombo naoloka nyanja, nkukafika ku mzinda wakwao. |
| 2 |
| Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.” |
| 3 |
| Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.” |
| Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi |