|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
AROMA 1:1 | PAULO, kapolowa Yesu Kristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu, | | AROMA 1:4 | amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu; | | AROMA 1:6 | mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Kristu; | | AROMA 1:7 | kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu. | | AROMA 1:8 | Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi. | | AROMA 2:16 | tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Kristu zinsinsi za anthu, monga mwa uthenga wanga wabwino. | | AROMA 3:22 | ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana; | | AROMA 3:24 | ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu; | | AROMA 3:26 | kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu, | | AROMA 4:24 | koma cifukwa ca ifenso, kwa ife amene cidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu, | | AROMA 5:1 | Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu; | | AROMA 5:11 | Ndipo si cotero cokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene talandira naye tsopano ciyanjanitso. | | AROMA 5:15 | Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa cifukwa ca kulakwa kwammodziyo, makamaka ndithu cisomo ca Mulungu, ndi mphatso yaulere zakucokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinacurukira anthu ambiri. | | AROMA 5:17 | Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu. | | AROMA 5:21 | kuti, mongaucimo unacita ufumu muimfa, comweconso cisomo cikacite ufumu mwa cilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. | | AROMA 6:3 | Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace? | | AROMA 6:11 | Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu. | | AROMA 6:23 | Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu. | | AROMA 7:25 | Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo. | | AROMA 8:1 | Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa. | | AROMA 8:2 | Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa. | | AROMA 8:11 | Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu. | | AROMA 8:34 | 9 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife. | | AROMA 8:39 | ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu. | | AROMA 10:9 | kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka: | | AROMA 13:14 | Koma bvalani inu Ambuye Yesu-Kristu, ndipo musaganizire za thupi kucita zofuna zace. | | AROMA 14:14 | Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa. | | AROMA 15:5 | Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu; | | AROMA 15:6 | kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu. | | AROMA 15:16 | kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. | | AROMA 15:17 | Cifukwa cace ndiri naco codzitamandira ca m'Kristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. | | AROMA 15:30 | Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine; | | AROMA 16:3 | Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu, | | AROMA 16:20 | Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse. | | AROMA 16:25 | Ndipo kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wanga wabwino, ndi kulalildra kwa Yesu Kristu, monga mwa bvumbulutso la cinsinsi cimene cinabisika mwa nthawi zonse zosayamba, | | AROMA 16:27 | kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen. | |
|