Mavesi a Baibulo Pamutuwu

Mitu
Mulungu
Khalidwe Labwino
Khalidwe Loipa
Machimo
Moyo
Mpingo
Zinsinsi
Angelo ndi Ziwanda
Zizindikiro za Masamu
Zowonjezera
Mulungu: [Dalitso]
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.
Mulungu adzatidalitsa; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye.
[24] Yehova akudalitse iwe, nakusunge; [25] Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. [7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
[7] Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. [8] Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Chifukwa mwa kudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo.
[16] nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako yekha, [17] kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;
[28] Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo. [29] Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
[1] Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. [2] Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. [3] Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
[1] Salimo la Davide. Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. [2] Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. [3] Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. [4] Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
[3] Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa. [4] Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Chewa Bible 1922
Bible Society of Malawi